Hymn 156

I love the Lord, the fount of life & grace

Author unknown

Verse 1

Ndikonda Mlungu pomva Mbuye wanga

Amva pemphero ndi kulira kwanga,

Namachereza khutu nditapfuula,

Andithandiza, nandipulumutsa.

Verse 2

Mulungu wanga ndiye wachifundo

Ndi wolungama mtima ndi wabwino;

Apulumtsa anthu akufoka,

Akathandiza nkhawa imachoka.

Verse 3

Mtimanga, bwera kuti upumule,

Wakuchitiranso zokoma Mbuye,

Wakuchotsera imfa ndi misozi,

Ndingakhumudwe asungira phazi.

Verse 4

Nditani ine kubwezera Mbuye

Zokoma zonse anandichitira?

Chipulumutso chake ndidzatama,

Ndinalumbira zija ndidzapatsa.

Verse 5

Imfa ya anthu ake imkomera,

Awalandira m’nyumba zokonzeka.

Mbuye, kapolo wanu ndipereka